Yeremiya 7:20 - Buku Lopatulika20 Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Nchifukwa chake ndidzaŵalanga koopsa mwaukali. Mkwiyo wanga udzagwera Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi mbeu zomwe. Mkwiyowo udzayaka ngati moto wosazimika.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika. Onani mutuwo |
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Monga mkwiyo wanga ndi ukali wanga wathiridwa kwa okhala mu Yerusalemu, momwemo ukali wanga udzathiridwa pa inu, pamene mudzalowa mu Ejipito; ndipo mudzakhala chitukwano, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, ndi chitonzo; ndipo simudzaonananso malo ano.