Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 5:4 - Buku Lopatulika

4 Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 5:4
23 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Wachita chiyani? Mau a mwazi wa mphwako andifuulira Ine kunthaka.


M'mwemo anafikitsa kwa Iye kufuula kwa osauka; ndipo anamva Iye kufuula kwa ozunzika.


Monga kapolo woliralira mthunzi, monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,


Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika.


popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo.


Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.


Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.


Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikulu ndi zokoma zopanda wokhalamo.


Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake;


Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.


Pakuti mwala wa m'khoma ufuula, ndi mtanda wa kuphaso udzauvomereza.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka.


Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima?


Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyire ife mbeu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.


Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo.


Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye mu Mwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa