Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 5:3 - Buku Lopatulika

3 Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 5:3
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati, Muluwu ndiwo mboni pakati pa ine ndi iwe lero. Chifukwa chake anatcha dzina lake, Galedi;


Muluwu ndiwo mboni, choimiritsachi ndicho mboni, kuti ine sindidzapitirira pa muluwu kunka kwa iwe, ndipo iwe sudzapitirira pa muluwu ndi pa choimiritsachi kudza kwa ine kuti tichitirane zoipa.


Ndipo Yakobo anaitana ana ake aamuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.


Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa, kuonda kwanga kundiukira, kuchita umboni pamaso panga.


Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pansonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.


Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.


inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.


Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda; ndi mitundu ya anthu idzayendako.


Ndipo kudzali m'masiku otsiriza, anena Mulungu, ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse, ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera, ndipo anyamata anu adzaona masomphenya, ndi akulu anu adzalota maloto;


Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;


ndipo mau ao adzanyeka chilonda; a iwo ali Himeneo ndi Fileto;


Ndipo Yoswa anati kwa anthu onse, Taonani, mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa; pakuti udamva mau onse a Yehova amene ananena kwa ife; ndipo udzakhala mboni yotsutsa inu, mungakanize Mulungu wanu.


ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,


Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, ndipo zidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, ndi kudya nyama yake, ndipo zidzampsereza ndi moto.


Ndipo ngati munthu sanapezedwe wolembedwa m'buku la moyo, anaponyedwa m'nyanja yamoto.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa