Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:1 - Buku Lopatulika

1 Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wamphesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kalanga ine! Ndasanduka ngati wokunkha wosapeza zotsalira. Sipadatsalenso mphesa zoti nkudya. Sipadatsaleko nkhuyu zimene ndimazikonda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:1
14 Mawu Ofanana  

Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!


Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?


Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.


Chifukwa chake padzakhala chotero pakati padziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo wa azitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ake.


Kuchokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa Ine! Amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.


ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiona wakupenya imeneyo, amaidya ili m'dzanja lake.


Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.


Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.


Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.


Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.


Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.


Zipatso zoyamba zonse zili m'dziko mwao, zimene amadza nazo kwa Yehova, zikhale zako; oyera onse a m'banja lako adyeko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa