Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mika 6:15 - Buku Lopatulika

15 Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Udzafesa koma osacheka; udzaponda azitona koma osadzola mafuta; udzaponda mphesa koma osamwa vinyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Mudzabzala, koma simudzakolola, Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzaŵadzola. Mudzaponda mphesa, koma vinyo wake simudzamulaŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mudzadzala, koma simudzakolola. Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito. Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.

Onani mutuwo Koperani




Mika 6:15
14 Mawu Ofanana  

Ndibzale ine nadye wina, ndi zondimerera ine zizulidwe.


Abzala tirigu, asenga minga; adzipweteka, koma osapindula kanthu, mudzakhala ndi manyazi a zipatso zanu, chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.


ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.


ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.


Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.


Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao;


Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.


Mwabzala zambiri, koma mututa pang'ono; mukudya, koma osakhuta; mukumwa, koma osakoledwa; mudziveka, koma palibe wofundidwa; ndi iye wolembedwa ntchito yakulipidwa alandirira kulipirako m'thumba lobooka.


Pakuti m'menemo chonenacho chili choona, Wofesa ndi wina, womweta ndi winanso.


nawamangira misasa, namaononga zipatso za m'dziko mpaka ufika ku Gaza, osawasiyira chochirira njala mu Israele, ngakhale nkhosa, kapena ng'ombe, kapena bulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa