Masalimo 97:1 - Buku Lopatulika1 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Chauta ndiye Mfumu, anthu a pa dziko lapansi akondwere, anthu onse a m'mbali mwa nyanja asangalale. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere. Onani mutuwo |
Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.