Masalimo 97 - Buku LopatulikaUlemerero wa ufumu wa Mulungu 1 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere; zisumbu zambiri zikondwerere. 2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu. 3 Moto umtsogolera, nupsereza otsutsana naye pozungulirapo. 4 Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu; dziko lapansi linaona nilinagwedezeka. 5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi. 6 Kumwamba kulalikira chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake. 7 Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu. 8 Ziyoni anamva nakondwera, nasekerera ana aakazi a Yuda; chifukwa cha maweruzo anu, Yehova. 9 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi, ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu ina yonse. 10 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa. 11 Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero oongoka mtima. 12 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi