Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 97:2 - Buku Lopatulika

2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wachifumu wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama, mu ufumu wake mulibe tsankho.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 97:2
18 Mawu Ofanana  

Musamatero ai, kupha olungama pamodzi ndi oipa, kuta olungama akhale monga oipa; musamatero ai; kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?


Pakuti adzachita chondiikidwiratu; ndipo zambiri zotere zili ndi Iye.


Atchingira pa mpando wake wachifumu, nayalapo mtambo wake.


Njira yanu inali m'nyanja, koyenda Inu nkumadzi aakulu, ndipo mapazi anu sanadziwike.


Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wanu wachifumu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.


Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova.


Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ndikudza kwa iwe mu mtambo wakuda bii, kuti anthu amve pamene ndilankhula ndi iwe, ndi kuti akuvomereze nthawi zonse. Pakuti Mose adauza Yehova mau a anthuwo.


Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukulu kuli Mulungu.


Kuchita mphulupulu kunyansa mafumu; pakuti mpando wao wakhazikika ndi chilungamo.


Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu; ndi wosamasula ndithu wopalamula; njira ya Yehova ili m'kamvulumvulu ndi mumkuntho; ndipo mitambo ndiyo fumbi la mapazi ake.


Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa