Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 97:7 - Buku Lopatulika

7 Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Onse opembedza milungu yonama, amene amanyadira mafano achabechabe, amachititsidwa manyazi, pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 97:7
19 Mawu Ofanana  

Mapiko a akerubi awa anafunyululika mikono makumi awiri; ndipo anaima ndi mapazi ao, ndi nkhope zao zinaloza kukhomo.


Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko.


Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.


Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.


Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.


kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.


Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.


Anthu onse ali opulukira ndi opanda nzeru; woyenga yense anyazitsidwa ndi fanizo lake losemasema; pakuti fanizo lake loyenga lili bodza, mulibe mpweya mwa iwo.


Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;


Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umenewo; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.


Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko;


Ndipo pamene atenganso wobadwa woyamba kulowa naye m'dziko, anena, Ndipo amgwadire Iye angelo onse a Mulungu.


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa