Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 97:11 - Buku Lopatulika

11 Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero oongoka mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Kuunika kufesekera wolungama, ndi chikondwerero oongoka mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Amaŵalira anthu amene amamumvera, ndipo anthuwo amakhaladi ndi chimwemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 97:11
17 Mawu Ofanana  

Ayuda anali nako kuunika, ndi kukondwera, ndi chimwemwe, ndi ulemu.


Ndipo moyo wako udzayera koposa usana; kungakhale kuli mdima kudzakhala ngati m'mawa.


Ukatsimikiza mtima kakuti, kadzakhazikikira iwe; ndi kuunika kudzawala panjira zako.


Kuunika kutulukira oongoka mtima mumdima; Iye ndiye wachisomo, ndi wansoni ndi wolungama.


Pakuti Inu muyatsa nyali yanga; Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.


Imbirani Mulungu, liimbireni nyimbo dzina lake; undirani mseu Iye woberekekayo kuchidikha; dzina lake ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi chimwemwe pamaso pake.


Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.


Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.


Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete, ndi chifukwa cha Yerusalemu sindidzapuma, kufikira chilungamo chake chidzatuluka monga kuyera, ndi chipulumutso chake monga nyali yoyaka.


Ndidzasenza mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndamchimwira, mpaka andinenera mlandu wanga, ndi kundiweruzira mlandu wanga; adzanditulutsira kwa kuunika, ndipo ndidzapenya chilungamo chake.


Ndadza Ine kuunika kudziko lapansi, kuti yense wokhulupirira Ine asakhale mumdima.


Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.


Ndipo pamzinda sipafunika dzuwa, kapena mwezi wakuuwalira; pakuti ulemerero wa Mulungu uunikira umenewu, ndipo nyali yake ndiye Mwanawankhosa.


Ndipo sikudzakhalanso usiku; ndipo sasowa kuunika kwa nyali, ndi kuunika kwa dzuwa; chifukwa Ambuye Mulungu adzawaunikira; ndipo adzachita ufumu kunthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa