Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 97:10 - Buku Lopatulika

10 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa. Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima. Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 97:10
38 Mawu Ofanana  

Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.


Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.


Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; koma ndikonda chilamulo chanu.


Yehova adzakusunga kukuchotsera zoipa zilizonse; adzasunga moyo wako.


Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.


Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.


Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.


Futuka pazoipa, nuchite zabwino, funa mtendere ndi kuulondola.


Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.


Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa.


kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake.


Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;


Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.


Koma Israele adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi chipulumutso chosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru kunthawi zosatha.


Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.


Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.


Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, chifukwa anandiona wosachimwa pamaso pake, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwe.


Iye apulumutsa, nalanditsa, nachita zizindikiro ndi zozizwa m'mwamba ndi padziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Daniele kumphamvu ya mikango.


Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena.


Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.


Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.


Pakuti chimene ndichita sindichidziwa; pakuti sindichita chimene ndifuna, koma chimene ndidana nacho, ndichita ichi.


Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi?


Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.


ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si onse ali nacho chikhulupiriro.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukavumbulutsidwa nthawi yotsiriza.


amene mungakhale simunamuone mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi chimwemwe chosaneneka, ndi cha ulemerero:


Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa