Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 96:13 - Buku Lopatulika

13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 idzayimba pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lonse mwachilungamo ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 96:13
16 Mawu Ofanana  

Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala chete. Moto udzanyeka pankhope pake, ndipo pozungulira pake padzasokosera kwakukulu.


Anthu akondwere, nafuule mokondwera; pakuti mudzaweruza anthu molunjika, ndipo mudzalangiza anthu padziko lapansi.


Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.


Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.


Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.


Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.


pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m'tsiku lija.


chotsalira wandiikira ine korona wa chilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ake.


akulindira chiyembekezo chodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkulu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu;


Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.


Ndipo ndinaona mutatseguka mu Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakumkwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nachita nkhondo molungama.


Ndipo ananena ndi ine, Usasindikiza chizindikiro mau a chinenero cha buku ili; pakuti nthawi yayandikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa