Masalimo 96 - Buku LopatulikaOnse a pansi pano ndi am'mwamba omwe alemekeze Mulungu ( 1Mbi. 16.23-33 ) 1 Muimbireni Yehova nyimbo yatsopano; muimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi. 2 Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. 3 Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu. 4 Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse. 5 Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba. 6 Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso. 7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu. 8 Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake. 9 Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa, njenjemerani pamaso pake, inu dziko lonse lapansi. 10 Nenani mwa amitundu, Yehova achita ufumu; dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke; adzaweruza mitundu ya anthu molunjika. 11 Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi; nyanja ibume mwa kudzala kwake. 12 Munda ukondwerere ndi zonse zili m'mwemo; pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzafuula mokondwera. 13 Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi