Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 96:3 - Buku Lopatulika

3 Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Fotokozerani ulemerero wake mwa amitundu; zodabwitsa zake mwa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 96:3
15 Mawu Ofanana  

Mlemekezeni chifukwa cha ntchito zake zolimba; mlemekezeni monga mwa ukulu wake waunjinji.


Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye, ndidzakuimbirani mwa mitundu.


Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


inde, ati, Chili chinthu chopepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israele; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale chipulumutso changa mpaka ku malekezero a dziko lapansi.


Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.


Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.


Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:


ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa