Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 96:2 - Buku Lopatulika

2 Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Muimbireni Yehova, lemekezani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 96:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.


Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mau ake, akumvera liu la mau ake.


Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu; ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova; ndi okondedwa anu adzakulemekezani.


Masiku onse ndidzakuyamikani; ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.


Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu.


Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake.


Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba paphiri lalitali; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena kumizinda ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!


Ndipo ananena nao, Mukani kudziko lonse lapansi, lalikirani Uthenga Wabwino kwa olengedwa onse.


Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa