Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 96:7 - Buku Lopatulika

7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tamandani, inu anthu a mitundu yonse, vomerezani kuti ulemerero ndi mphamvu, zonse nzake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 96:7
17 Mawu Ofanana  

Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukira nadzatembenukira kwa Yehova, ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


Kwa Iye kukhale mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.


ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.


Zitatha izi ndinamva ngati mau aakulu a khamu lalikulu mu Mwamba, lili kunena, Aleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;


Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, ndi kunena, Aleluya; pakuti achita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.


Ndipo cholengedwa chilichonse chili m'mwamba, ndi padziko, ndi pansi padziko, ndi m'nyanja, ndi zonse zili momwemo, ndinazimva zilikunena, Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi mphamvu, kufikira nthawi za nthawi.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa