Masalimo 63 - Buku LopatulikaMtima woliralira kuyanjana ndi Mulungu Salimo la Davide; muja anakhala m'chipululu cha Yuda. 1 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga; ndidzakufunani m'matanda kucha. Moyo wanga ukumva ludzu la kwa Inu, thupi langa lilirira Inu, m'dziko louma ndi lotopetsa, lopanda madzi. 2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera. 3 Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. 4 Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu. 5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera. 6 Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku. 7 Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu. 8 Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza. 9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge, adzalowa m'munsi mwake mwa dziko. 10 Adzawapereka kumphamvu ya lupanga; iwo adzakhala gawo la ankhandwe. 11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; yense wakulumbirira iye adzatamandira; pakuti pakamwa pa iwo onena bodza padzatsekedwa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi