Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 63:8 - Buku Lopatulika

8 Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 63:8
19 Mawu Ofanana  

Ndipo m'ntchito iliyonse anaiyamba mu utumiki wa nyumba ya Mulungu, ndi m'chilamulo, ndi m'mauzo, kufuna Mulungu wake, anachita ndi mtima wake wonse, nalemerera nayo.


Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.


Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.


Ndipo ine, mundigwirizize mu ungwiro wanga, ndipo mundiike pankhope panu kunthawi yamuyaya.


Koma ndikhala ndi Inu chikhalire, mwandigwira dzanja langa la manja.


Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.


Pamene ndinati, Literereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.


Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu, dzanja lake lamanja ndi kundifungatira.


Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mzinda, m'makwalala ndi m'mabwalo ake, ndimfunefune amene moyo wanga umkonda: Ndimfunafuna, koma osampeza.


Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.


Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.


kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa