Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 63:2 - Buku Lopatulika

2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Kuti ndione mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, monga ndinakuonani m'malo oyera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 63:2
19 Mawu Ofanana  

Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthawi zonse.


Funani Yehova, ndi mphamvu yake; funsirani nkhope yake nthawi zonse.


Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova.


Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu.


Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Misozi yanga yakhala ngati chakudya changa, usana ndi usiku; pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse, Mulungu wako ali kuti?


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu.


Anapenya mayendedwe anu, Mulungu, mayendedwe a Mulungu wanga, mfumu yanga, m'malo oyera.


napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.


Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.


Ulemerero wa Lebanoni udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a Kachisi wanga; ndipo ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.


Ndipo ndikhutitsa moyo wa ansembe ndi mafuta, ndipo anthu anga adzakhuta ndi zokoma zanga, ati Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa