Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 63:9 - Buku Lopatulika

9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge, adzalowa m'munsi mwake mwa dziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Koma iwo amene afuna moyo wanga kuti auononge, adzalowa m'munsi mwake mwa dziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Koma anthu amene amayesayesa kuwononga moyo wanga, adzatsikira ku dziko la anthu akufa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 63:9
20 Mawu Ofanana  

Uwakwirire pamodzi m'fumbi, uzimange nkhope zao pobisika.


Mwandipondetsa patalipatali, sanaterereke mapazi anga.


Achite manyazi, nadodome iwo akukondwera chifukwa cha choipa chidandigwera. Avekeke ndi manyazi ndi kupunzika iwo akudzikuza pa ine.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.


Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa.


Imfa iwagwere modzidzimutsa, atsikire kumanda ali amoyo, pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao.


Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira kudzenje la chionongeko. Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku ao sadzafikira nusu; koma ine ndidzakhulupirira Inu.


Achite manyazi, nadodome amene afuna moyo wanga. Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe amene akonda kundichitira choipa.


Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.


Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu.


Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe, pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.


Koma udzatsitsidwa kunsi kumanda, ku malekezero a dzenje.


Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.


Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.


alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.


Ngakhale anauka anthu kukulondolani, ndi kufuna moyo wanu, koma moyo wa mbuye wanga udzamangika m'phukusi la amoyo lakukhala ndi Yehova Mulungu wanu; koma Iye adzaponya miyoyo ya adani anu kuwataya monga chotuluka m'choponyera mwala.


Ndiponso Yehova adzapereka Israele pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisraele m'dzanja la Afilisti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa