Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 63:5 - Buku Lopatulika

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi chonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mudzandikhutitsa ndi zonona, ndipo ndidzakutamandani ndi mau osangalala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona. Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 63:5
17 Mawu Ofanana  

Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga: ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.


Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova.


Kwezani manja anu kumalo oyera, nimulemekeze Yehova.


Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino; muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.


Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m'chilungamo, ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.


Kuti ndipite kufikira guwa la nsembe la Mulungu, kufikira Mulungu wa chimwemwe changa chenicheni, ndi kuti ndikuyamikeni ndi zeze, Mulungu, Mulungu wanga.


Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.


Milomo yanga idzafuula mokondwera poimbira Inu nyimbo; inde, moyo wanga umene munaombola.


Pamaso pake pali ulemu ndi ukulu. M'malo opatulika mwake muli mphamvu ndi zochititsa kaso.


Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.


Ndipo m'phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.


Ndidzamangitsanso mudzi wako, ndipo udzamangidwa, iwe namwali wa Israele; udzakometsedwanso ndi mangaka, ndipo udzatulukira masewero a iwo akukondwerera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa