Masalimo 16 - Buku LopatulikaMunthu wokhulupirira Mulungu akhazikika mtima, osaopa kutayika Mikitamu wa Davide. 1 Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu. 2 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu. 3 Za oyera mtima okhala padziko lapansi, iwo ndiwo omveka mbiri, mwa iwowo muli chikondwero changa chonse. 4 Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga. 5 Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa, ndinu wondigwirira cholandira changa. 6 Zingwe zandigwera mondikondweretsa; inde cholowa chokoma ndili nacho. 7 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza. 8 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. 9 Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika. 10 Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde. 11 Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi