Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 16:2 - Buku Lopatulika

2 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndimamuuza Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga. Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga; popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 16:2
15 Mawu Ofanana  

Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.


Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.


Ndili ndi yani Kumwamba, koma Inu? Ndipo padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.


Yehova, Ambuye wathu, dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi! Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.


Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.


Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.


Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu Ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzatchula dzina lanu.


Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Chotero inunso m'mene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.


Tomasi anayankha nati kwa Iye, Ambuye wanga, ndi Mulungu wanga.


Ndipo anayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzambwezeranso?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa