Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 16:7 - Buku Lopatulika

7 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu, usikunso impso zanga zindilangiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndikutamanda Chauta amene ali phungu wanga. Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu; ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 16:7
20 Mawu Ofanana  

Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu.


Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova, ndipo ndinasamalira chilamulo chanu.


Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka, pakuphunzira maweruzo anu olungama.


Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.


Mulungu wanga, ndiitana usana, koma simuvomereza; ndipo usiku, sindikhala chete.


Koma usana Yehova adzalamulira chifundo chake, ndipo usiku nyimbo yake idzakhala ndi ine. Inde pemphero la kwa Mulungu wa moyo wanga.


Pokumbukira Inu pa kama wanga, ndi kulingalira za Inu maulonda a usiku.


Pakuti mtima wanga udawawa, ndipo ndinalaswa mu impso zanga;


Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.


Tsiku la nsautso yanga ndinafuna Ambuye. Dzanja langa linatambalika usiku, losaleka; mtima wanga unakana kutonthozedwa.


Ndikumbukira nyimbo yanga usiku; ndilingalira mumtima mwanga; mzimu wanga unasanthula.


Ndine mwini uphungu ndi kudziwitsa; ndine luntha; ndili ndi mphamvu.


Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.


Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israele, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.


Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.


Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.


Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa impso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zake, monga zipatso za ntchito zake.


Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.


Ndipo ndidzaononga ana ake ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti Ine ndine Iye amene ayesa impso ndi mitima; ndipo ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa ntchito zanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa