Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 16:6 - Buku Lopatulika

6 Zingwe zandigwera mondikondweretsa; inde cholowa chokoma ndili nacho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Zingwe zandigwera mondikondweretsa; inde chosiyira chokoma ndili nacho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 16:6
13 Mawu Ofanana  

Mudzatalikitsa moyo wa mfumu. Zaka zake zidzafikira mibadwomibadwo.


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.


chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.


Yesu ananena naye, Usandikhudze, pakuti sinditha kukwera kwa Atate; koma pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kunka kwa Atate wanga, ndi Mulungu wanu.


ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.


ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,


ngati tipirira, tidzachitanso ufumu ndi Iye: ngati timkana Iye, Iyeyunso adzatikana ife:


Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa