Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 16:4 - Buku Lopatulika

4 Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina. Sindidzathira nsembe zao zamwazi, ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Amene amasankhula milungu ina, amadzichulukitsira mavuto. Sindidzatsira nawo nsembe zao zamagazi kapena kutchula maina a milungu yaoyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 16:4
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anaimiritsa mwala pamalo pamene ananena ndi iye, choimiritsa chamwala: ndipo anathira pamenepo nsembe yothira, nathirapo mafuta.


Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.


Onse akutumikira fano losema, akudzitamandira nao mafano, achite manyazi: Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.


Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.


Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?


Koma inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mulungu wamwai gome, ndi kudzazira mulungu waimfa zikho za vinyo wosakaniza;


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu ina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.


Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.


Iwo osamalira mabodza opanda pake ataya chifundo chaochao.


osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kutchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa