Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 119:16 - Buku Lopatulika

16 Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ndimakondwera ndi malamulo anu; sindidzayiwala konse mawu anu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 119:16
24 Mawu Ofanana  

Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.


Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu.


Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse.


Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu.


Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.


Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; pakuti sindiiwala chilamulo chanu.


Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.


Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu.


Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa, ndizo zondipangira nzeru.


Mundiyendetse mopita malamulo anu; pakuti ndikondwera m'menemo.


Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu, amene ndiwakonda.


Anandikulunga nazo zingwe za oipa; koma sindinaiwale chilamulo chanu.


Mtima wao unona ngati mafuta; koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.


Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo; popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.


Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira; koma sindiiwala malemba anu.


kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.


Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama; koma kuwaononga akuchita mphulupulu.


Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga;


Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.


Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa