Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:18 - Buku Lopatulika

18 Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:18
80 Mawu Ofanana  

Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.


Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu wolingana ndi Inu m'thambo la kumwamba, kapena padziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,


Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa chisomo ndi chifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye.


Ndipo mverani mapembedzero a kapolo wanu ndi a anthu anu Israele, popemphera iwo kuloza konkuno; ndipo mumvere Inu mu Mwamba mokhala Inumo, ndipo pakumva Inu, mukhululukire.


nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.


Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye.


Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Mphulupulu zinandipambana; koma mudzafafaniza zolakwa zathu.


Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu.


Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zazikulu, akunga Inu ndani, Mulungu?


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.


Pakuti kuli yani kuthambo timlinganize ndi Yehova? Afanana ndi Yehova ndani mwa ana a amphamvu?


Yehova, Mulungu wa makamu, wamphamvu ndani wonga Inu, Yehova? Ndipo chikhulupiriko chanu chikuzingani.


Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?


Ndipo anati, Ngati ndapeza ufulu tsopano pamaso panu, Ambuye, ayendetu Ambuye pakati pa ife; pakuti awa ndi anthu opulupudza; ndipo mutikhululukire mphulupulu ndi uchimo wathu, ndipo mutilandire tikhale cholowa chanu.


Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbuu.


Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani?


Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Ine ndafafaniza monga mtambo wochindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo machimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.


woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.


Unatopa ndi njira yako yaitali; koma sunanene, Palibe chiyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; chifukwa chake sunalefuke.


Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.


Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako aamuna adzakukwatira iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.


Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu.


Ndipo ndidzasangalala mu Yerusalemu, ndi kukondwera mwa anthu anga; ndipo mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula.


Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.


Kodi adzasunga mkwiyo wake kunthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka chimaliziro? Taona, wanena ndi kuchita zoipa monga unatero.


Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.


ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.


Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.


Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.


Ebedemeleki anatuluka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,


Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.


koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.


Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? Ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Zoipa zake zilizonse anazichita sizidzakumbukika zimtsutse, anachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo ndithu.


Ambuye Mulungu wathu ndiye wachifundo, ndi wokhululukira; pakuti tampandukira Iye;


Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.


Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.


Ndipo kudzachitika kuti aliyense adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa; pakuti m'phiri la Ziyoni ndi mu Yerusalemu mudzakhala chipulumutso, monga Yehova anatero, ndi mwa otsala amene Yehova adzawaitana.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Edomu, kapena zinani, sindidzabweza kulanga kwake; popeza analondola mphwake ndi lupanga, nafetsa chifundo chake chonse, ndi mkwiyo wake unang'amba ching'ambire nasunga mkwiyo wake chisungire;


Ndipo Yehova anati kwa ine, Amosi, uona chiyani? Ndipo ndinati, Chingwe cholungamitsira chilili. Nati Ambuye, Taona, ndidzaika chingwe cholungamitsira chilili pakati pa anthu anga Israele, sindidzawalekanso:


Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.


Ndipo anapemphera kwa Yehova, nati, Ha, Yehova! Si ndiwo mau anga ndikali m'dziko langa? Chifukwa chake ndinafulumira kuthawira ku Tarisisi, pakuti ndinadziwa kuti Inu ndinu Mulungu wachisomo ndi wodzala chifundo, wolekerera ndi wokoma mtima mochuluka, ndi woleka choipacho.


Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.


ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m'phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha.


Chifukwa chake Iye adzawapereka kufikira nthawi yoti wobalayo wabala; pamenepo otsala a abale ake adzabwera pamodzi ndi ana a Israele.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.


Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.


Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.


Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng'ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.


ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.


Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu aamuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadire Baala.


Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe, wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza, ndi pa mitambo mu ukulu wake.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.


Pamenepo anachotsa milungu yachilendo pakati pao, natumikira Yehova; ndipo mtima wake unagwidwa chisoni chifukwa cha mavuto a Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa