Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:17 - Buku Lopatulika

17 Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Adzanyambita fumbi ngati njoka; ngati zokwawa za padziko, adzanjenjemera potuluka m'ngaka mwao; adzafika kwa Yehova Mulungu wao ndi mantha, nadzaopa chifukwa cha iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Adzavimvinizika pa dothi ngati njoka, ngati zolengedwa zina zokwaŵa. Adzabwera ali njenjenje kuchokera ku malinga ao. Moopa adzatembenukira kwa Inu Chauta, Mulungu wathu, ndipo adzachita nanu mantha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Adzabwira fumbi ngati njoka, ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi. Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo; mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu ndipo adzachita nanu mantha.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:17
27 Mawu Ofanana  

Alendo adzafota, nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.


Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati.


Alendo adzafota, nadzatuluka monjenjemera m'ngaka mwao.


Inde mafumu onse adzamgwadira iye, amitundu onse adzamtumikira.


Okhala m'chipululu adzagwadira pamaso pake; ndi adani ake adzaluma nthaka.


Muwachititse mantha, Yehova; adziwe amitundu kuti ali anthu.


Chifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mzinda wa mitundu yakuopsa udzakuopani Inu.


Ndipo mafumu adzakulera, ndi akazi ao aakulu adzakuyamwitsa; iwo adzakugwadira ndi nkhope zao zoyang'ana pansi, nadzaseteka fumbi la m'mapazi ako: ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndi iwo amene alindira Ine sadzakhala ndi manyazi.


Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kuti amitundu anthunthumire pamaso panu.


Mmbulu ndi mwanawankhosa zidzadyera pamodzi; ndi mkango udzadya udzu ngati ng'ombe; ndi fumbi lidzakhala chakudya cha njoka; sizidzapwetekana, kapena kusakazana m'phiri langa lonse lopatulika, ati Yehova.


Ndipo zidzafika ndi kutera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.


Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.


Aike kamwa lake m'fumbi; kapena chilipo chiyembekezo.


Pamenepo mudzathawa kudzera chigwa cha mapiri anga; pakuti chigwa cha mapiri chidzafikira ku Azali; ndipo mudzathawa monga umo munathawira chivomezi, masiku a Uziya mfumu ya Yuda; ndipo Yehova Mulungu wanga adzadza, ndi opatulika onse pamodzi ndi Inu.


Adzaonda nayo njala adzanyekeka ndi makala a moto, chionongeko chowawa; ndipo ndidzawatumizira mano a zilombo, ndi ululu wa zokwawa m'fumbi.


Ndipo anamyankha Yoswa nati, Popeza anatiuzitsa akapolo anu kuti Yehova Mulungu wanu analamulira mtumiki wake Mose kukupatsani dziko lonseli, ndi kupasula nzika zonse za m'dziko pamaso panu; potero tinaopera kwambiri moyo wathu pamaso panu, ndipo tinachita chinthuchi.


Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa