Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mika 7:16 - Buku Lopatulika

16 Amitundu adzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Amitundu adzaona nadzachita manyazi ndi mphamvu yao yonse; adzagwira pakamwa, m'makutu mwao mudzagontha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo adzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzangogwira pakamwa, ndi kutseka makutu motaya mtima.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzagwira pakamwa pawo ndipo makutu awo adzagontha.

Onani mutuwo Koperani




Mika 7:16
17 Mawu Ofanana  

Ndiyang'anireni, nimusumwe, gwirani pakamwa panu.


Taonani, ndakhululuka ine, ndidzakubwezerani mau otani? Ndigwira pakamwa.


Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati kwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.


Ngati wapusa podzikweza, ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.


Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.


momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.


Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.


Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziwika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo alauli adzachita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama; pakuti kuyankha kwa Mulungu kulibe.


Ndipo otsala a Yakobo adzakhala mwa amitundu, pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mkango mwa nyama zakuthengo, ngati msona wa mkango mwa magulu a nkhosa; umenewo ukapitako, upondereza, numwetula, ndipo palibe wakupulumutsa.


ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ndidzayesa kuononga amitundu onse akudza kuyambana ndi Yerusalemu.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Ndipo amitundu anakwiya, ndipo unadza mkwiyo wanu, ndi nthawi ya akufa yakuti aweruzidwe, ndi yakupereka mphotho akapolo anu aneneriwo, ndi oyera mtima, ndi iwo akuopa dzina lanu, ang'ono ndi akulu; ndi kuononga iwo akuononga dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa