Masalimo 21 - Buku LopatulikaDavide ayamika Mulungu pa kugonjetsa adani Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu! 2 Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake, ndipo simunakane pempho la milomo yake. 3 Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma; muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake. 4 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye; mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi. 5 Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu; mumchitira iye ulemu ndi ukulu. 6 Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse; mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu. 7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye. 8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse, dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu. 9 Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu. Yehova adzawatha m'kukwiya kwake, ndipo moto udzawanyeketsa. 10 Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa padziko lapansi, ndi mbeu zao mwa ana a anthu. 11 Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita. 12 Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao. 13 Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu; potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi