Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 21:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova, ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Paja mfumuyo imakhulupirira Chauta, ndipo siidzagwedezeka chifukwa cha chikondi chosasinthika cha Wopambanazonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Pakuti mfumu imadalira Yehova; kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba, iyo sidzagwedezeka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 21:7
17 Mawu Ofanana  

Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu; mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.


Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.


Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.


Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.


Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.


Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.


Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu; ndidzaimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.


Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.


Ndiponso, Ndidzamtama Iye. Ndiponso, Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa