Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 21:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti mudzawabweza m'mbuyo, popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 pakuti idzaŵapirikitsa potendekera nkhope zao ndi mauta ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 21:12
11 Mawu Ofanana  

Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani, Inu wodikira anthu? Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu? Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?


Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa; inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.


Ndipo adani anga mwawalozetsa m'mbuyo kwa ine, kuti ndipasule ondidawo.


Mutibwereretsa kuthawa otisautsa, ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.


Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.


Koma Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa.


Pobwerera m'mbuyo adani anga, akhumudwa naonongeka pankhope panu.


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Wathifula uta wake, nandiyesa polozetsa muvi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa