Masalimo 65 - Buku LopatulikaDavide alemekeza Mulungu pa madalitso ochuluka Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide. Nyimbo. 1 Mu Ziyoni akulemekezani Inu mwachete, Mulungu, adzakuchitirani Inu chowindachi. 2 Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu. 3 Mphulupulu zinandipambana; koma mudzafafaniza zolakwa zathu. 4 Wodala munthuyo mumsankha, ndi kumyandikizitsa, akhale m'mabwalo anu. Tidzakhuta nazo zokoma za m'nyumba yanu, za m'malo oyera a Kachisi wanu. 5 Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja. 6 Ndinu amene mukhazikitsa mapiri ndi mphamvu yanu; pozingidwa nacho chilimbiko. 7 Amene atontholetsa kukuntha kwa nyanja, kukuntha kwa mafunde ake, ndi phokoso la mitundu ya anthu. 8 Ndipo iwo akukhala kumalekezero adzachita mantha chifukwa cha zizindikiro zanu; mukondweretsa apo patulukira dzuwa, ndi apo lilowera. 9 Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeretsa kwambiri; mtsinje wa Mulungu udzala nao madzi, muwameretsera tirigu m'mene munakonzera nthaka. 10 Mukhutitsa nthaka yake yolima; mufafaniza nthumbira zake; muiolowetsa ndi mvumbi; mudalitsa mmera wake. 11 Muveka chakachi ndi ukoma wanu; ndipo mabande anu akukha zakucha. 12 Akukha pa mabusa a m'chipululu; ndipo mapiri azingika nacho chimwemwe. 13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi