Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 65:13 - Buku Lopatulika

13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Podyetsa mpodzaza ndi zoweta; ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu; zifuula mokondwera, inde ziimbira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Madambo adzaza ndi zoŵeta, zidikha zadzaza ndi dzinthu, zonsezo zikufuula ndi kuimbira limodzi mwachimwemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Madambo akutidwa ndi zoweta ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu; izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 65:13
17 Mawu Ofanana  

Pakuti aweruza nazo mitundu ya anthu apatsa chakudya chochuluka.


Kuti nkhokwe zathu zidzale, kutipatsa za mitundumitundu; ndi kuti nkhosa zathu ziswane zikwizikwi, inde zikwi khumi kubusako.


M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebanoni, ndipo iwo a m'mizinda adzaphuka ngati msipu wapansi.


Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.


ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.


Imbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wachichita icho; kuwani inu, mbali za pansi padziko; imbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; chifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israele.


Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.


Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.


Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.


Ndipo kusekera ndi kukondwa kwachotsedwa, kumunda wobala ndi kudziko la Mowabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kufuula; kufuula sikudzakhala kufuula.


Musamaopa, nyama zakuthengo inu; pakuti m'chipululu muphukanso msipu; pakuti mitengo ibala zipatso zao; mikuyu ndi mipesa ipatsa mphamvu zao.


Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.


Koma sanadzisiyire Iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa