Dziko lauzimu lilipoli, ndipo mmenemo timayenera kuchita nkhondo ndi pemphero komanso ndi mawu a Mulungu. Nkhondo zazikulu zimamenyedwa m’dziko lauzimu limeneli. M’dziko lauzimuli ndi kumene mphamvu zodabwitsa za Mulungu zimaonekera. Si kumene timangomenyana ndi mizimu yoipa yokha ayi, komanso kumene umapezera zodabwitsa ndi chipambano m’moyo wako.
Pakuti nkhondo yathu si yolimbana ndi anthu, koma ndi olamulira, ndi akuluakulu, ndi mafumu a dziko la mdima lino, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba. (Aefeso 6:12) Apa Mulungu akutiuza za dziko lauzimu limeneli, kumene ukhoza kupambana pokhapokha wodzazidwa ndi mphamvu zake.
Ngakhale kuti timakhala m’dzikoli, sitimenya nkhondo monga mmene dziko limamenyera. Zida zathu za nkhondo si za dziko lino, koma zili ndi mphamvu ya Mulungu yogumula mipanda. (2 Akorinto 10:3-4)
musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwake kumchitira choipa munthu mnzake.
Chifukwa chake atero Woyera wa Israele, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo; chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.
Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi, ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo. Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao; omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.
phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.
Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israele kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aejipito awapsinja nako.
Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu; Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya; monga ndachitira Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake? Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa. Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu; dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye. Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo. Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto. Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi. Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yake, ndi wa m'munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera. Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yake idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera. kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!
Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi; wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.
Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.
Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato;
Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.
Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?
Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao. Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu. Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake. Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu. Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera. Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake. Chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndilingirira choipa pa banja ili, chimene simudzachotsako makosi anu, kapena kuyenda modzikuza inu; pakuti nyengo iyi ndi yoipa.
Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.
Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.
Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.
Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu; kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Ejipito. Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;
Mulungu, mokhala mwake moyera, ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.
Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu. Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.
Yehova wa makamu atero. Ana a Israele ndi ana a Yuda asautsidwa pamodzi; ndipo onse amene anawagwira ndende awagwiritsitsa; akana kuwamasula. Mombolo wao ngwa mphamvu; dzina lake Yehova wa makamu: adzawanenera mlandu wao ndithu; kuti apumutse dziko lapansi, nadzidzimutse okhala mu Babiloni.
Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.
Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao mu Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.
Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.
Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.
Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa chisoni chako, ndi nsautso yako, ndi ntchito yako yovuta, imene anakugwiritsa, Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa. Lira, chipata iwe; fuula, mzinda iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake. Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira. pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!
Ndipo ndidzadyetsa iwo amene atsendereza iwe ndi nyama yaoyao; ndi mwazi waowao; iwo adzaledzera monga ndi vinyo wotsekemera; anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndili Mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.
Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali mu Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.
Apulumutsa aumphawi kulupanga la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu. Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo, ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.
Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse. Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.
Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi. Yehova apenyetsa osaona; Yehova aongoletsa onse owerama; Yehova akonda olungama. Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.
Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilime lao lilephera, chifukwa cha ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israele sindidzawasiya.
Apulumutsa wozunzika mwa kuzunzika kwake, nawatsegulira m'khutu mwao mwa kupsinjika kwao.
Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.
Muimbire Yehova, mulemekeze Yehova; pakuti walanditsa moyo wa aumphawi m'dzanja la ochita zoipa.
Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.
Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholowa chanu. Amapha wamasiye ndi mlendo, nawapha ana amasiye.
Kondwera kwambiri, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula mwana wamkazi wa Yerusalemu; taona, Mfumu yako ikudza kwa iwe; ndiye wolungama, ndi mwini chipulumutso; wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi mwana wamphongo wa bulu.
Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.
Koma achepanso, nawerama, chifukwa cha chisautso, choipa ndi chisoni. Anasokera m'chipululu, m'njira yopanda anthu; osapeza mzinda wokhalamo. Atsanulira chimpepulo pa akulu, nawasokeretsa m'chipululu mopanda njira. Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.
Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu; waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza?
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato; ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;
Potero anawaikira akulu a misonkho kuti awasautse ndi akatundu ao. Ndipo anammangira Farao mizinda yosungiramo chuma, ndiyo Pitomu ndi Ramsesi. Koma monga momwe anawasautsiramo, momwemo anachuluka, momwemonso anafalikira. Ndipo anavutika chifukwa cha ana Israele. Ndipo Aejipito anawagwiritsa ana a Israele ntchito yosautsa; nawawitsa moyo wao ndi ntchito yolimba, ya dothi ndi ya njerwa, ndi ntchito zonse za pabwalo, ntchito zao zonse zimene anawagwiritsa nzosautsa.
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine. Pomwepo olungama adzamyankha Iye kuti, Ambuye, tinakuonani Inu liti wanjala, ndi kukudyetsani? Kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinaona Inu liti mlendo, ndi kukucherezani? Kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu? koma anzeruwo anatenga mafuta m'nsupa zao, pamodzi ndi nyali zao. Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.
Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Ndipo chiweruziro chabwerera m'mbuyo, ndi chilungamo chaima patali; pakuti choona chagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe. Inde choona chisoweka; iye amene asiya choipa, zifunkhidwa zake; ndipo Yehova anaona ichi, ndipo chidamuipira kuti palibe chiweruzo.
Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Ili ndi gawo la munthu woipa kwa Mulungu, ndi cholowa cha akupsinja anzao achilandira kwa Wamphamvuyonse. Akachuluka ana ake, ndiko kuchulukira lupanga, ndi ana ake sadzakhuta chakudya. Akumtsalira iye adzaikidwa muimfa, ndi akazi ake amasiye sadzalira maliro. Chinkana akundika ndalama ngati fumbi, ndi kukonzeratu zovala ngati dothi; azikonzeretu, koma wolungama adzazivala, ndi wosalakwa adzagawa ndalamazo.
Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu. Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa? Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.
Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wampesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu; muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye, Yehova wa makamu.
Pakuti goli la katundu wake, ndi mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womsautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midiyani.
Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake;
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti, Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga; kuti tigule osauka ndi ndalama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu. Yehova walumbira pali kudzikuza kwa Yakobo, Ngati ndidzaiwala konse ntchito zao zilizonse?
Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha, ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Chiwawa sichidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa. Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona. Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako. Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda. Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova. Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa. Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make. Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu; Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu. Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamuwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m'mtima mwake. Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe. Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga. Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao. Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe. M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako. Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao. Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo zakuthengo zingakuchulukire. kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.
Pakuti ndinapulumutsa wozunzika wakufuula; mwana wamasiye yemwe wosowa mthandizi. Dalitso la iye akati atayike linandidzera, ndi mtima wa mkazi wamasiye ndinauimbitsa mokondwera. Ndinavala chilungamo, ndipo chinandivala ine; chiweruzo changa chinanga mwinjiro ndi nduwira. Ndinali maso a akhungu, ndi mapazi a otsimphina. Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa. Ndipo ndinathyola nsagwada ya wosalungama, ndi kukwatula chogwidwa kumano kwake.
Opirikitsidwa a Mowabu akhale ndi iwe, khala iwe chomphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.
Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake; ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m'malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo; ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya.
Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.
Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamuwerengera phindu. Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma polowa dzuwa uchibwezere kwa iye; popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo.
Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma. Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu.
Popeza adzaima padzanja lamanja la waumphawi, kumpulumutsa kwa iwo akuweruza koipa moyo wake.
Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.
Koma atero Yehova, Ngakhale am'nsinga a wamphamvu adzalandidwa, ndi chofunkha cha woopsa chidzapulumutsidwa; pakuti Ine ndidzakangana naye amene akangana ndi iwe, ndipo ndidzapulumutsa ana ako.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipo adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova. Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.
Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake. Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lake silili logontha, kuti silingamve; Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tiphunthwa usana monga m'chizirezire; tili m'malo amdima ngati akufa. Tonse tibangula ngati zilombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira chiweruziro koma palibe; tiyang'anira chipulumutso koma chili patali ndi ife. Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso pa Inu, ndipo machimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu zili ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa; ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima. Ndipo chiweruziro chabwerera m'mbuyo, ndi chilungamo chaima patali; pakuti choona chagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe. Inde choona chisoweka; iye amene asiya choipa, zifunkhidwa zake; ndipo Yehova anaona ichi, ndipo chidamuipira kuti palibe chiweruzo. Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; chifukwa chake mkono wakewake unadzitengera yekha chipulumutso; ndi chilungamo chake chinamchirikiza. Ndipo anavala chilungamo monga chida chapachifuwa, ndi chisoti cha chipulumutso pamutu pake; navala zovala zakubwezera chilango, navekedwa ndi changu monga chofunda. Monga mwa ntchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ake ukali, nadzabwezera adani ake chilango; nadzabwezeranso zisumbu chilango. Chomwecho iwo adzaopa dzina la Yehova kuchokera kumadzulo, ndi ulemerero wake kumene kutulukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati chigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa. koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva.
Anthu a m'dziko anazunzazunza, nalandalanda mwachiwawa, napsinja ozunzika ndi aumphawi, nazunza mlendo wopanda chifukwa. Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mzinda wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao. Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe. Chifukwa chake ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yaoyao ndinaibweza pamutu pao, ati Ambuye Yehova.
kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo. Ndipo Mulungu anamva kubuula kwao, ndi Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo. Ndipo Mulungu anapenya Aisraele, ndi Mulungu anadziwa.
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.
ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.
Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika, nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa. Oongoka mtima adzachiona nadzasekera; koma chosalungama chonse chitseka pakamwa pake.
koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.
koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.
Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m'chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo.
Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima; Anthu awiri anakwera kunka ku Kachisi kukapemphera; winayo Mfarisi ndi mnzake wamsonkho. Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu; ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndili nazo. Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa. Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, wosati uja ai; pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa. Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere. Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu. Ndipo mkulu wina anamfunsa Iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizichita chiyani, kuti ndilowe moyo wosatha? Koma Yesu anati kwa iye, Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu. nanena, M'mzinda mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu. Udziwa malamulo. Usachite chigololo, Usaphe, Usabe, Usachite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amai ako. Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga. Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa chinthu chimodzi: gulitsa zilizonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni mu Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine. Koma pakumva izi anagwidwa nacho chisoni chambiri; pakuti anali mwini chuma chambiri. Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali. Koma akumvawo anati, Tsono ndani angathe kupulumutsidwa? Koma Iye anati, Zinthu zosatheka ndi anthu zitheka ndi Mulungu. Ndipo Petro anati, Taonani ife tasiya zathu za ife eni, ndipo takutsatani Inu. Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum'bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, Ndipo m'mzinda momwemo munali mkazi wamasiye; ndipo anadza kwa iye nanena, Mundiweruzire mlandu pa wotsutsana nane. koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi ino; ndipo m'nthawi ilinkudza moyo wosatha. Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri. Pakuti adzampereka kwa amitundu, nadzamseka, nadzamchitira chipongwe, nadzamthira malovu; ndipo atamkwapula adzamupha Iye; ndipo tsiku lachitatu adzauka. Ndipo sanadziwitse kanthu ka izi; ndi mau awa adawabisikira, ndipo sanazindikire zonenedwazo. Ndipo kunali, pamene anayandikira ku Yeriko, msaona wina anakhala m'mbali mwa njira, napemphapempha; ndipo pakumva khamu la anthu alinkupita, anafunsa, Ichi nchiyani? Ndipo anamuuza iye, kuti, Yesu Mnazarayo alinkupita. Ndipo anafuula, nanena, Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. Ndipo iwo akutsogolera anamdzudzula iye, kuti akhale chete; koma iye anafuulitsa chifuulire, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo. Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu; Ndipo Yesu anaima, nalamulira kuti abwere naye kwa Iye; ndipo m'mene adafika pafupi, anamfunsa iye, Ufuna ndikuchitire chiyani? Ndipo anati, Ambuye, kuti ndipenyenso. Ndipo Yesu anati kwa iye, Penyanso: chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye, ndi kulemekeza Mulungu: ndipo anthu onse pakuona, anachitira Mulungu mayamiko. koma chifukwa cha kundivuta ine mkazi wamasiye amene ndidzamweruzira mlandu, kuti angandilemetse ndi kudzaidza kwake. Ndipo Ambuye anati, Tamverani chonena woweruza wosalungama. Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?
Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopirikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndikulimbitsa yodwalayo; koma yonenepa ndi yolimba ndidzaziononga, ndidzazidyetsa ndi chiweruzo.
Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.
Ndipo ndinati, Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israele; simuyenera kodi kudziwa chiweruzo? Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi chisalungamo. Akulu ake aweruza chifukwa cha mphotho, ndi ansembe ake aphunzitsa chifukwa cha malipo, ndi aneneri ake alosa chifukwa cha ndalama; koma atsamira pa Yehova, nati, Kodi Yehova sali pakati pa ife? Palibe choipa chodzatigwera. Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango. Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao; inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika. Pamenepo adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthawi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe ao.
Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.