Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 140:12 - Buku Lopatulika

12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 140:12
16 Mawu Ofanana  

pamenepo mverani Inu mu Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.


pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao mu Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao,


anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lao.


Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira;


amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?


Pakuti sanapeputse ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Adzaweruza ozunzika a mwa anthu, adzapulumutsa ana aumphawi, nadzaphwanya wosautsa.


Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga; mwakhala pa mpando wachifumu, woweruza wolungama.


Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi, ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.


koma ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi chibonga cha kukamwa kwake, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.


Iye anaweruza mlandu wa aumphawi ndi osowa; kumeneko kunali kwabwino. Kodi kumeneko si kundidziwa Ine? Ati Yehova.


akhungu alandira kuona kwao, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa