Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 140:13 - Buku Lopatulika

13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu, ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 140:13
15 Mawu Ofanana  

Sasunga woipa akhale ndi moyo, koma awaninkha ozunzika zowayenera iwo.


Pakuti Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama; woongoka mtima adzapenya nkhope yake.


Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.


Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.


Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.


Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?


Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira mu ulemerero.


Kondwerani mwa Yehova, olungama inu; ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.


Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao; omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.


Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; chifukwa oterowo adzadya zipatso za machitidwe ao.


Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.


Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.


pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa