Masalimo 140 - Buku LopatulikaDavide apempha Mulungu amlanditse kwa mdani woipa wamphamvu Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide. 1 Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; 2 amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo. 3 Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri. 4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga. 5 Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe. 6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova. 7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo. 8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye; musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze. 9 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga, choipa cha milomo yao chiwaphimbe. 10 Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso. 11 Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse. 12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi. 13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi