Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 140:3 - Buku Lopatulika

3 Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Amanola lilime lao kuti likhale ngati la njoka, m'kamwa mwao muli ululu wa mamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka; pa milomo yawo pali ululu wa mamba. Sela

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 140:3
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anati kwa mkaziyo, Chiyani chimene wachitachi? Ndipo anati mkaziyo, Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Ululu wao ukunga wa njoka; akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwake.


Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani?


Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.


Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka, najompha ngati mamba.


zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.


ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.


Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.


Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa.


milomo ya akutsutsana nane ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.


Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.


Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa