Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 140:7 - Buku Lopatulika

7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa, munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Inu Chauta, Ambuye anga, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mwateteza moyo wanga pa tsiku lankhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 140:7
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anaika maboma mu Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.


Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.


Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.


Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu chandikuza ine.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.


Ndidzaimbira zakukulemekezani Inu, mphamvu yanga; pakuti Mulungu ndiye msanje wanga, Mulungu wa chifundo changa.


Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.


Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.


Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.


Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.


Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa