Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 140:6 - Buku Lopatulika

6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga; munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndimauza Chauta kuti, “Inu ndinu Mulungu wanga,” tcherani khutu kuti mumve liwu la kupemba kwanga, Inu Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.” Imvani kupempha kwanga Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 140:6
18 Mawu Ofanana  

Ndimkonda, popeza Yehova amamva mau anga ndi kupemba kwanga.


Yehova ndiye gawo langa: Ndinati ndidzasunga mau anu.


Ambuye, imvani liu langa; makutu anu akhale chimverere mau a kupemba kwanga.


Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.


Ndinafuulira kwa inu, Yehova; ndinati, Inu ndinu pothawirapo panga, gawo langa m'dziko la amoyo.


Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.


Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga, ndilibe chabwino china choposa Inu.


Koma ine ndakhulupirira Inu, Yehova, ndinati, Inu ndinu Mulungu wanga.


Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.


Imvani Mulungu, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani.


Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.


Mfuu umvekedwe m'nyumba zao, pamene muwatengera khamu la nkhondo dzidzidzi; pakuti akumba dzenje lakundigwira ine, anabisira mapazi anga misampha.


Moyo wanga uti, Gawo langa ndiye Yehova; chifukwa chake ndidzakhulupirira.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa