Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 141:1 - Buku Lopatulika

1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Ndikukuitanani, Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Tcherani khutu kuti mumve liwu langa pamene ndikupemphera kwa Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 141:1
10 Mawu Ofanana  

Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga ndi kundichotsera mphulupulu yanga? Popeza tsopano ndidzagona kufumbi; mudzandifunafuna, koma ine palibe.


Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.


Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Koma Inu, Yehova, musakhale kutali; mphamvu yanga Inu, mufulumire kundithandiza.


Mverani mau a kupemba kwanga, pamene ndilirira Inu, pamene ndikweza manja anga kuloza ponenera panu poyera.


Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova.


Achite manyazi, nadodome amene afuna moyo wanga. Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe amene akonda kundichitira choipa.


Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; mundifulumirire, Mulungu. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga; musachedwe, Yehova.


Musandikhalire kutali, Mulungu; fulumirani kundithandiza, Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa