Masalimo 141 - Buku LopatulikaDavide apempha Mulungu amthandize poyesedwa ndi zoipa Salimo la Davide. 1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine; munditcherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu. 2 Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo. 3 Muike mdindo pakamwa panga, Yehova; sungani pakhomo pa milomo yanga. 4 Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao. 5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera. 6 Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe; nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa. 7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda, monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi. 8 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye; ndithawira kwa Inu; musataye moyo wanga. 9 Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake. 10 Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao, kufikira nditapitirira ine. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi