Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 141:4 - Buku Lopatulika

4 Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa, ndisadzipereke ku ntchito zoipa pamodzi ndi anthu ochita zoipa, ndisadye nawo maphwando ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 141:4
21 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.


Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.


Nati, Ndidzatuluka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ake onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; tuluka, ukatero kumene.


kuti atitembenuzire kwa Iye yekha mitima yathu iyende m'njira zake zonse, ndi kusunga malamulo ake onse ndi malemba ake ndi maweruzo ake, amene anawalamulira makolo athu.


Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai.


Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.


Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.


popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.


Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.


Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.


koma Yehova sanakupatseni mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.


Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu:


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa