Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 141:5 - Buku Lopatulika

5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Munthu wolungama angathe kundimenya kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo, koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa, pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 141:5
23 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, pakulankhula naye mfumu, inanena naye, Takuika kodi ukhale wopangira mfumu? Leka, angakukanthe. Pamenepo mneneriyo analeka, nati, Ndidziwa kuti Mulungu watsimikiza mtima kukuonongani, popeza mwachita ichi ndi kusamvera kupangira kwanga.


Chitirani chokoma, Yehova, iwo okhala okoma; iwo okhala oongoka mumtima mwao.


Mundiyalikira gome pamaso panga m'kuona kwa adani anga; mwandidzoza mutu wanga mafuta; chikho changa chisefuka.


Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu.


Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.


Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.


Chitsiru chipeputsa mwambo wa atate wake; koma wosamalira chidzudzulo amachenjera.


Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera; nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.


Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.


Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.


Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.


Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.


koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;


Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa