Yeremiya 22:3 - Buku Lopatulika3 Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Chautatu akuti uziweruza molungama ndi mosakondera. Munthu amene adambera zake uzimpulumutsa kwa womsautsa. Usavutitse mlendo, mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye. Usakhetse magazi a anthu osachimwa pa malo ano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. Onani mutuwo |