Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 22:2 - Buku Lopatulika

2 ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 ‘Iwe mfumu ya ku Yuda, imva mau a Chauta. Imva iwe amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide, iweyo pamodzi ndi atumiki ako ndiponso anthu ako amene amaloŵera pa zipata izi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 22:2
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Chifukwa chake tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wake wachifumu, ndi khamu lonse lakumwamba lili chilili m'mbali mwake, ku dzanja lamanja ndi lamanzere.


Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.


Chifukwa chake imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a mu Yerusalemu.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Nenani kwa mfumu ndi kwa amake wa mfumu, Dzichepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.


nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.


Yehova atero: Tsikira kunyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,


Pakuti ngati mudzachitadi ichi pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera m'magaleta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ake, ndi anthu ake.


Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndachotsa mu Yerusalemu kunka ku Babiloni.


Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mzindawu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;


Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.


Ima m'chipata cha nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.


Chifukwa chake abusa inu, imvani mau a Yehova:


Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;


Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa