Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 3:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsono ndidzakufikani pafupi kuti ndikuzengeni mlandu. Mosataya nthaŵi ndidzanena mau otsutsa mfiti, anthu achigololo, a umboni wonama, odyerera antchito ao, ovutitsa akazi ndi ana amasiye, ochita alendo zosalungama ndipo onse amene sandiwopa Ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”

Onani mutuwo Koperani




Malaki 3:5
63 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Pakuti ndicho moto wakunyeka mpaka chionongeko, ndi chakuzula zipatso zanga zonse.


Monga kapolo woliralira mthunzi, monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,


Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake.


Tamvani, anthu anga, ndidzakuchitirani mboni; Israele, ukadzandimvera!


Pamaso pa Yehova, pakuti akudza; pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndi mitundu ya anthu ndi choonadi.


Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi chilungamo, ndipo mitundu ya anthu molunjika.


Koma anamwino anaopa Mulungu, ndipo sanachite monga mfumu ya Aejipito inawauza, koma analeka ana aamuna akhale ndi moyo.


Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;


Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.


Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.


Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.


Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.


Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama.


Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


pakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akuchotseni inu m'dziko lanu, kunka kutali kuti ndikupirikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.


Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babiloni;


chifukwa anachita zopusa mu Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.


Pamenepo iwo anati kwa Yeremiya, Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika pakati pa ife, ngati sitichita monga mwa mau onse Yehova Mulungu wanu adzakutumizani nao kwa ife.


Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.


Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?


Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.


Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.


Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamutu pao.


Ndipo munthu wakutembenukira kwa obwebweta ndi anyanga kuwatsata ndi chigololo, nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndipo ndidzamsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake.


Imvani, mitundu ya anthu, inu nonse; tamvera, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo; ndipo Ambuye Yehova akhale mboni yakutsutsa inu, Ambuye mu Kachisi wake wopatulika.


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Ndipo ndinanena nao, Chikakomera inu, ndipatseni mphotho yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphotho yanga, kulemera kwake masekeli a siliva makumi atatu.


Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?


Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.


Mwalemetsa Yehova ndi mau anu. Koma mukuti, Tamlemetsa ndi chiyani? Ndi ichi chakuti munena, Yense wakuchita choipa ali wokoma pamaso pa Mulungu, ndipo akondwera nao; kapena, Ali kuti Mulungu wa chiweruzo?


Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku?


Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.


Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu;


Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.


Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;


Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.


Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa amene atchula pachabe dzina lakelo.


asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.


Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.


Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro.


Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa