Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 3:4 - Buku Lopatulika

4 Pamenepo chopereka cha Yuda ndi Yerusalemu chidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Pamenepo chopereka cha Yuda ndi Yerusalemu chidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Choncho nsembe za Yuda ndi za Yerusalemu zidzakondweretsa Chauta, monga zidaaliri masiku amakedzana.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 3:4
22 Mawu Ofanana  

Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la chipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.


Nakwerako Solomoni ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku chihema chokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza chikwi chimodzi.


Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.


Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe paguwa lanu la nsembe.


naonso ndidzanka nao kuphiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa paguwa langa la nsembe; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.


Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa